Showing posts with label Nthano. Show all posts
Showing posts with label Nthano. Show all posts

Tuesday, June 17, 2008

MALODZA A HALISONI

Wolemba: Pacharo F. Munthali

Halisoni adamwetulira akudzisilira pakalilore. Tindevu tonga tonde tidali njo! Pachibwano chake. Kachingwe konga chikwanje kadali ndi! Pakhosi pake. Jekete loti mbu! lidali pholipholi

“Bambo, ntenthandevu wapsya,” Adatero mkazi wandodai.

“Ndikubwera mayi,” adayankha Halisoni.
Apa malingaliro adadzala m’mutu mwa ndodai ndipo misozi idamanga ufumu mu malingaliro ake. Izi zidali chomwechi pokumbukira m’mene adavutikira kuti afike pomwe adali leropa.

Makolo a Halisoni adamwali iye ali ndi zaka zitatu pangozi ya galimoto. Izi zidapangitsa kuti adzikhala ndi agogo ake aakazi aNaphiri. Apa nkuti agogo ake aamuna atatsamilanso nkono

Koma patatha zaka zitatu, nao aNaphiri adatsikira kulichete. Ndipo mikwingwirimayi idadzetsa theng’eneng’e m’moyo wa Halisoni. Zokhomazi monga ichitira mvula ya matalala ukaukulunga mpala, zidapangitsa Halisoni kuti sukulu ayisiye mufolomu ya chiwiri.

Pang’onopang’no ngati tsokonombwe, Halisoni adapeza ntchito pakampani yowotcherera zitsulo mu tawuni ya Wakwithu.

Podziwa kuti fodya wako ndi amene ali pamphuno, Halisoni amagwira ntchito ndi mtima wake wonse. Izi zidachititsa kuti adzikwezedwa maudindo pafupipafupi.

Pokhala kuti pakampanipo azungu amakondapo kwambiri, iwo akamabwerere kwao katundu wao ankasiyira Halisoni. Chifukwa cha ichi, Halisoni adakhala munthu wopata. Adali ndi galimoto komanso nyumba yolozeka ndipo samasowa kanthu pakhomo pake.

“Bambo tiyi akuziziratu kuno.” Adamukumbutsa chomwecho mkazi wake wa Halisoni.

Atathana naye kazutsayo Halisoni adauyatsa ulendo wakuntchito monga mwachizolowezi.

Kuchoka tsiku lomwe mzungu wina wake waku Kosovo adamusiyira njinga ya moto chifukwa cha luntha lake pakagwiridwe ka ntchito anthu ambiri amamuchitira dumbo.

Koma iye sadalabade, m’malo mwake adapitiriza kugwira ntchito mothetsa makhang’a. Iye amachita izi podziwa kuti kulimbikira kulibe mlowam’malo.

Iye adali ndi ntchito yowonetsetsa kuti zinthu zonse zili bwino nthawi yotsegula kapena kutseka ikafika.

Ngakhale zinthu zimayenda mwa myaa! chomwechi, padali chipsinjo chimodzi pakampanipo chomwe chimamulondalonda ngati chithuzithunzi. Chipsinjocho ndiye Chidyangu, yemwe adali wachiwiri kwa iye.

Chidyangu adali ndi mbiri osati yongododometsa komanso yoopsya. Iye pokhala munthu woti ndi wachipembezo chimodzi ndi bwana, nthawi zambiri ndi bwanayo amakhala limodzi. Mukutero chilichonse iye anganene bwanayo ankangovomereza.

Nthawi zambiri Halisoni amada nkhawa kuti mwina mutu wake utupa akamaganiza za Chidyangu.

Halisoni alichiyendere ulendo wakuntchito, ntima wake udagunda mwadzidzi. Malingaliro atsiku lotsatiralo adamufikira. Adakumbuka kuti dzulo lakero adasiira Chidyangu makiyi akuntchito pamene anadwala mwadzidzi ndipo adaweluka mofulumira. Nthawi imeneyi nkuti bwana wankulu pakampanipo atapita ku Jubeki ndipo amayembekezeredwa kubwera tsiku limeneli. Chomwe chidamuwawa kwambiri chidali choti bwana adanenetsa kuti makiyi asamasiyire aliyense kupatula bwanayo. Chidali chachidziwikire kuti bwana akamva izi akhala wokwiya kwambiri.

Patsikuli akufika kuntchito mtima wake udadayamba kugunda modetsa nkhawa ngati utuluka m’chimake. Nalo thupi lidachita tsemwe ngati mwanapiye wogwera m’chithaphwi. Nkhawa yasasimbika idamupeza Poona anthu pantchitopo ali khumakhuma ngati abongololo onamizira kufa ndipo nkhope zawo zidavala chisoni.
Halisoni adayetsetsa kufulumira poyenda koma kungwangwangwa kwa maondo ake kudamuchitira njiru. Apa adadziwiratu kuti zinthu zasolobana

“Bambo Halisoni, tafotokozani za zomwe zachitika apazi.” Adatero bwana wankulu pakampanipo. Nthawi imeneyi nkuti atangofika kumene kuchokera ku South africa. Zitseko za maofesi a pakampanipo zidali zitathyoledwa, ndipo katundu wambiri adakwangwanulidwa. Halisoni adangoima kusowa chonena ngati waphonya penate. Sadakhulupilire zomwe maso ake ankaona.

“Ndi-ndi-ndi-ndidamusiyira Chi-chi-dyangu,” adayankha mwachibwibwi, ndipo m’maso muli gwa! bwanayo adamuuza Halisoni kuti yake yawuma. Kukhala ngati kutokosola pabala ndi kamtengo pa dzino lobooka, Halisoni adauzidwa kuti katundu wake alandidwa kuti akagulitsidwe pobwezeretsa katundu yemwe wabetsa.

Halisoni adazweta mutu, ndipo chokamba chidamusowa monga momwe achitira mwana akaona kholo lake likubuula chifukwa cholumidwa ndi mavu.Adadziwa kuti Chidyangu adamuyenda pansi ndipo sadakayike. Kwa iye dziko lidachita chipidigoli. Nacho chimdima cha nzanga ali pati chidadzinga m’maso mwake ndipo sadakhulupilire zomwe zinkachitikazo. Adaona ngati kutulo.

Mwadzidzi, adagwa pansi ngati thumba la kachewere, ndipo adakomoka nthawi yomweyo.

ZANGA NZOWAWA

Wolemba Pacharo Felix Munthali
Ooo! ndikusowa poyambira ee!
Ndiri ku sekondale ndi anzanga timakonda kukambirana zambiri zokhuza tsogolo lathu. Nthawi zambiri podziwa kuti nkhanga zidapangana atambala asanakokolike, timakambirana zomwe tidzachite mtsogolo. Chimodzi mwa chinthu chomwe timakambirana chidali chokhuza ana angati omwe timafuana kuti tizakhale nawo mu banja. Pagulu lathu lonse ine ndi amene ndidali ndi masomphenya angaanga popeza ndimafuna ana osaponsera awiri pamene anzanga ambiri amafuna ana monga asanu nkumapita uko.
"Ha! inu ndiye ayi, wina akazagundidwa ndi maminibasi othamanga ngati akambukuwa, komanso winayo nkupenga ndi chamba chomwe anyamata amasiku ano akukwemba za inu ndiye zizathera pomwepo basi," Chidzete, m'modzi mwa anzanga amandinyogodola chomwecho nthawi zambiri.
Koma zomwe ndikuona lero, ha! ngati kuti khoswe wa moyo akuchokera mkamwa mwa m'busa ulariki uli mkati – zododometsa inu. Ndikuona ngati kuti dziko landida. Ndipo wanga ndikuona ngati ndi wakung'anjo yamoto basi poti ndingowaganizira zoipa anzanga makamaka anamageyaanyezi, inde anamamina yogati, ee!
Kukamacha kwa anthu ena odala tsiku lawo limakhala loti aphe makwacha kuonjezera upwepwete paukhumutcha wawo. Kukhala kwa ine, ntchito ikumakhala yoika ubongo wanga kukhalira m'mphanthi makamaka poganizira m'mene ndingapondere lamphawi, inde kupha matambala oti mwina nkudyako matemba m'malo mwantoliro.
Za ine oo! ndizovuta kufotokoza. Ine ndimati maloza, koma mkazi wanga akumazitcha mbonaona. Koma abale...
M'mawa tikamatuluka m'nyumba – ine, mkazi wanga komanso ana anga timakhala ngati kuti timu ya mpira wamiyendo kuphatikizapo anthu okhala pa benchi, kuli kukula kwa banja. Ndipo tikamatuluka mapoto kunzanso masupuni zimakhala zikusokosa ngati masapota ampira wa miyendo.
Abale! nditayamba bizinesi yokhoza njinga zoonongeka zakapalasa, zinthu kunena mwachindunji sizimandiyendera ingakhale pang'ono. Amayi anga adali okhuzidwa kwambiri. Pachifukwa ichi adayamba kuyetsayetsa njira zoti ine zinthu zindiyendere.
Apa ndi pamene tsiku lina munthu wangongole atandilanda zipangizo zopangira bizinesi yanga amayi adandiwuza za sing'anga ogona pamoto dzuwa likuswa mtengo osatuluka thukuta ingakhale pang'ono, eee! Adandiwuza kuti wachokera ku Tanzania. Adandisina khutu pondimemeza kuti iwo adapita kwa sing'angayo kuti akaombeze ndikuona ngati nane ndizakhalepo munthu woyenda tang'atang'a tayi atasanduka lamba.
Pamayambiriro ndimakana, koma ntibu wamavuto utandionetsa chomwe chidaletsa nkhuku kuseka ndidalola ndikupita kwa sing'angayo.
"Koma mterawu, ukagwiretse ntchito tsiku lomwe m'banja lako muzabadwe mwana wamkazi. Ukamwere pa mphambano, utapolamira chakumpoto," adatero sing'anga wakuArushayo.
Nkakumbuka zonsezi nyanja ya chisoni imapanga mafunde m'mtima mwanga. Lero ndine munthu woti ndiri ndi ana khumi komanso awiri. Kuonjezera apo, mkazi wanga ndiwoyembekezera. Kudikira chuma...
Ndayetsayetsa kumwa mtera uwu komanso uwo, koma tsoka iro palibe kusintha kwa ntundu wina kulikonse. Mwana wamkazi akusowa, ee! Komanso pamene mkazi wanga wafika zoti akhoza kuberekanso ndizoyikitsa moyo wake pachiswe cholusa.
Kumayadi konse ndikutamidwa osati ndikukhala ndi ana amphongo omwe angokhalira kumenyana, komanso mavuto omwe amadza kamba kakuchulukana kwa anawa.
Popeza kuti bizinesi siyimayenda ndidachiona kuti ndi chanzeru kuyamba kaye ntchito pamene ndikudikirira mwana wa mkazi. Apa ndipamene ndidapeza ntchito kwa Ahindirira, mwenye waku India.
Pokhala pamapeto pa mwezi, ndikantchito komwe ndimagwira kwa Ahindirira ana anayi adali akudikirira ndalama zoti akalipire ku sukulu zawo za sekondale. Naye amene ndidali ndingongole yake ya chimanga adali ataopsyeza kuti ngati sindimpatsa ndalama mwezi uno azanditenthera nyumba pamodzi ndi ana anga. Nawo ana apulayimale amafuna kundipomboneza kuti akuti ndiwapatse ndalama zoti aziripirira alonda. Awa ndidangowauza kuti akaone sitayiro kusulu konko, ee! Azikathawathawa, uku akumwa phala laurere, ee!
Pamene ndikuyandikira nyumba yanga, panthawiyi nkuti nthawi iri chamumanayini koloko ya usiku, ndikumva kulira konga ngati kuti munthu ali mu ululu wazaoneni, ee! Kodi ndi chiani? Ndiwachimanga? Ndidayiwalira amene timapanga nawo lendi nyumba adandiuza kuti ngati sindimupatsa ndalama lero andichotsa.
Koma ndisanakhote, anyamata azitho ngati kuti amakakha ndege, akundikanyanga pakhosi. Kenako ndalama zonse zapita. Ndikumva kulira kwa mkazi wanga, koma ndikulephera kuzuka. Andibaya ndi mpeni. Kuli phokoso loopsya.