Wolemba Pacharo Felix Munthali
Ooo! ndikusowa poyambira ee!
Ndiri ku sekondale ndi anzanga timakonda kukambirana zambiri zokhuza tsogolo lathu. Nthawi zambiri podziwa kuti nkhanga zidapangana atambala asanakokolike, timakambirana zomwe tidzachite mtsogolo. Chimodzi mwa chinthu chomwe timakambirana chidali chokhuza ana angati omwe timafuana kuti tizakhale nawo mu banja. Pagulu lathu lonse ine ndi amene ndidali ndi masomphenya angaanga popeza ndimafuna ana osaponsera awiri pamene anzanga ambiri amafuna ana monga asanu nkumapita uko.
"Ha! inu ndiye ayi, wina akazagundidwa ndi maminibasi othamanga ngati akambukuwa, komanso winayo nkupenga ndi chamba chomwe anyamata amasiku ano akukwemba za inu ndiye zizathera pomwepo basi," Chidzete, m'modzi mwa anzanga amandinyogodola chomwecho nthawi zambiri.
Koma zomwe ndikuona lero, ha! ngati kuti khoswe wa moyo akuchokera mkamwa mwa m'busa ulariki uli mkati – zododometsa inu. Ndikuona ngati kuti dziko landida. Ndipo wanga ndikuona ngati ndi wakung'anjo yamoto basi poti ndingowaganizira zoipa anzanga makamaka anamageyaanyezi, inde anamamina yogati, ee!
Kukamacha kwa anthu ena odala tsiku lawo limakhala loti aphe makwacha kuonjezera upwepwete paukhumutcha wawo. Kukhala kwa ine, ntchito ikumakhala yoika ubongo wanga kukhalira m'mphanthi makamaka poganizira m'mene ndingapondere lamphawi, inde kupha matambala oti mwina nkudyako matemba m'malo mwantoliro.
Za ine oo! ndizovuta kufotokoza. Ine ndimati maloza, koma mkazi wanga akumazitcha mbonaona. Koma abale...
M'mawa tikamatuluka m'nyumba – ine, mkazi wanga komanso ana anga timakhala ngati kuti timu ya mpira wamiyendo kuphatikizapo anthu okhala pa benchi, kuli kukula kwa banja. Ndipo tikamatuluka mapoto kunzanso masupuni zimakhala zikusokosa ngati masapota ampira wa miyendo.
Abale! nditayamba bizinesi yokhoza njinga zoonongeka zakapalasa, zinthu kunena mwachindunji sizimandiyendera ingakhale pang'ono. Amayi anga adali okhuzidwa kwambiri. Pachifukwa ichi adayamba kuyetsayetsa njira zoti ine zinthu zindiyendere.
Apa ndi pamene tsiku lina munthu wangongole atandilanda zipangizo zopangira bizinesi yanga amayi adandiwuza za sing'anga ogona pamoto dzuwa likuswa mtengo osatuluka thukuta ingakhale pang'ono, eee! Adandiwuza kuti wachokera ku Tanzania. Adandisina khutu pondimemeza kuti iwo adapita kwa sing'angayo kuti akaombeze ndikuona ngati nane ndizakhalepo munthu woyenda tang'atang'a tayi atasanduka lamba.
Pamayambiriro ndimakana, koma ntibu wamavuto utandionetsa chomwe chidaletsa nkhuku kuseka ndidalola ndikupita kwa sing'angayo.
"Koma mterawu, ukagwiretse ntchito tsiku lomwe m'banja lako muzabadwe mwana wamkazi. Ukamwere pa mphambano, utapolamira chakumpoto," adatero sing'anga wakuArushayo.
Nkakumbuka zonsezi nyanja ya chisoni imapanga mafunde m'mtima mwanga. Lero ndine munthu woti ndiri ndi ana khumi komanso awiri. Kuonjezera apo, mkazi wanga ndiwoyembekezera. Kudikira chuma...
Ndayetsayetsa kumwa mtera uwu komanso uwo, koma tsoka iro palibe kusintha kwa ntundu wina kulikonse. Mwana wamkazi akusowa, ee! Komanso pamene mkazi wanga wafika zoti akhoza kuberekanso ndizoyikitsa moyo wake pachiswe cholusa.
Kumayadi konse ndikutamidwa osati ndikukhala ndi ana amphongo omwe angokhalira kumenyana, komanso mavuto omwe amadza kamba kakuchulukana kwa anawa.
Popeza kuti bizinesi siyimayenda ndidachiona kuti ndi chanzeru kuyamba kaye ntchito pamene ndikudikirira mwana wa mkazi. Apa ndipamene ndidapeza ntchito kwa Ahindirira, mwenye waku India.
Pokhala pamapeto pa mwezi, ndikantchito komwe ndimagwira kwa Ahindirira ana anayi adali akudikirira ndalama zoti akalipire ku sukulu zawo za sekondale. Naye amene ndidali ndingongole yake ya chimanga adali ataopsyeza kuti ngati sindimpatsa ndalama mwezi uno azanditenthera nyumba pamodzi ndi ana anga. Nawo ana apulayimale amafuna kundipomboneza kuti akuti ndiwapatse ndalama zoti aziripirira alonda. Awa ndidangowauza kuti akaone sitayiro kusulu konko, ee! Azikathawathawa, uku akumwa phala laurere, ee!
Pamene ndikuyandikira nyumba yanga, panthawiyi nkuti nthawi iri chamumanayini koloko ya usiku, ndikumva kulira konga ngati kuti munthu ali mu ululu wazaoneni, ee! Kodi ndi chiani? Ndiwachimanga? Ndidayiwalira amene timapanga nawo lendi nyumba adandiuza kuti ngati sindimupatsa ndalama lero andichotsa.
Koma ndisanakhote, anyamata azitho ngati kuti amakakha ndege, akundikanyanga pakhosi. Kenako ndalama zonse zapita. Ndikumva kulira kwa mkazi wanga, koma ndikulephera kuzuka. Andibaya ndi mpeni. Kuli phokoso loopsya.
Tuesday, June 17, 2008
Subscribe to:
Post Comments (Atom)
No comments:
Post a Comment