Monday, July 21, 2008

UFULU WATHU NDI UMENEWU, KOMA...

Wolemba Pacharo Felix Munthali
Pa 6 July monga dziko, tidali ndi mwambo wokumbukira tsiku lomwe tidalandira ufulu wodzilamulira kuchokera m’manja mwa asamunda dzaka makumi anayi kuzanso zinayi zapitazo.

Tsikuli pokhala kuti ndi lomwe timakondwerera ufulu wozilamulira, ndi limodzi mwa matsiku ochepetsetsa kwambiri pakalendala yomwe anthu osiyanasiyana, angasiyane bwanji, amabwera pamodzi. Ndi tsiku lomwe anthu mungadane bwanji – kaya kamba kosiyana zipani, zipembezo ndi zina zotero – mumakhala pamodzi.

Kunena zoona zomwe pulezidenti Bingu wa Mutharika adanena ku Mzuzu zoti anthu tonse tiyenera kukhala pamodzi ndi zoona kwambiri. Ndi chinthu choti wina aliyense ayenera kukhuzidwa m’mtima kuti ayenera kutenga nawo mbali pa mwambo wa pamwamba, womwe pophatikizapo kuzetsa umodzi pakati pa anthu, umalemekeza anthu amene adatengapo mbali pozetsa ufulu wozilamulira womwe tikukondwa nawo lerowu.

Iyi ndi nthawi yomwe anthu poiwala mkwiyo woza munjira zosiyansiyana, amabwera pamodzi ngati anthu afuko limodzi la Malawi. Apa sizimadabwitsa kuona anthu akuvina magule osiyanasiyana. Ndipo kuonetsa umodzi anthu amabwera ndi magule osiyanasiyana kuyambira kuchokera kumpoto kukathera ku m’mwera.

Kuonjezera apo zomwe zimachitika nthawi yokondwerera tsiku lomwe tidalandiara ufulu wozilamulira zimakhala ngati kuphera mphongo zomwe nyimbo ya fuko lathu imanena zoti anthu timapempha mulungu kuti tiokhale pa mtendere. Ndipo mtendere umabwera ngati anthu nonse mukhala ngati anthu amodzi.

Komano, poona m’mene mwambowu udachitikira – pena pake udali ngati kuti udali mwambo wachipani cha Democratic Progressive Party (DPP). Kuyambira azimayi a Bingu kukhathera akuluakulu a boma kunsanja onse mavalidwe awo adali osonyeza ngati kuti udali nsonkhano wa DPP. Zidali zodabwitsa kuona mwambo wa boma anthu akuvala mochititsa kaso koma mwachisoni atavala chomwecho pa mwambo waukulu wa dziko ngati umenewu.

Chomwe ndikuziwa ndi chakuti anthu amene amachokera m’madera osiyanasiyana sikuti iwowa amakhala kuti ndi amene amapangitsa mwambowu. Amakauzidwa nthawi zambiri. Ndipo mbiri yawonetsa kuti ambiri amene amavina panthawiyi sikuti ndi anthu wamba, ayi sizikhala choncho. Ambirio amene amakaviana amakhala anthu omweomwewo amene amavina nthawi ya zipani. Koma uwu pokhala mwambo waukulu chidakakhala cha nzeru kuti anthuwa adakawauza m’mene amayenera kuvalira. Kodi anthuwa akuluakulu a zipani zawozi samawauza zoti komwe amapitaku sudali nsokhano wachipani, koma ndi mwambo wa boma ndiye mavalidwe ayenera kukhala otere?

Pamwambowo pulezidenti wathu adazuzula atsogoleri azipani zotsutsa boma chifukwa chosaonekera pa mwambo wa pamwamba komanso wofunika ku mtundu wa Malawi. Inde anthu timafunika kukhala okonda dziko lathu. Ndipo kukhala nawo pa mwambo onga umenewu ndi kofunika kwambiri. Komano chovuta ndichakuti, kodi m’mene mwambowu udaliri, kodi anthu ngati a Tembo kapena a Muluzi adakakhala nawo pa mwambowu ndi mautoto a DPP ali ponseponse adakaona mwambowo ngati wa boma kapena DPP? Komanso pokhala anthu andale zidakawasangalatsa kuona zotero?

Kuonjezera apo, potengera m’mene a Tembo adawakuwira ku Dedza, kodi munthu wotero adakakhalanso ndi chilakolako choti akakhalenso pamwambo wa boma? Atsogoleri otsutsa boma adakhala ngati kuti adalakwitsadi, koma m’mene a pulezidenti athu amalankhulira, anthu ena akuti, njondazi pena pake zidachita bwino.

Inde mwina mwake tidakakhala ndi malamulo a m’mene ziyera kukhalira zidakakhala bwino. Chomwe ndikutanthawuza ndichakuti, pali njira ziwiri zomwe titha kukondwerera mwambo waukulu ngati umenewu. Yoyamba ndikukhala ndi malamulo oti nthawi yamwambo ngati umenewu, mtundu wachipani chilichonse usamapezeke. Koma ngati njiora imeneyi siingatheke, ndiye anthu ena akuona ngati anthu onse kaya ndi otsutsa kaya a boma onse azivala mtundu uliwonse akufuna.

Kunena mwachindunji, mwambuwu uyenera kukhala phunziro ku boma komanso zipani zonse, kuti iwo ayenera kusiyanitsa kuti mwambo wa boma komanso wachipani ndi zinthu ziwiri zosiyana. Kunena mosazambayitsa zomwe zimakonda kuchitika pa zochitika za boma pokhala ngati ndi nsonkhano wa chipani kamba ka mitundu yochulukitsitsa ya zipani ndi m’nyozo ku mbendera ya fuko lathu.

Ingoganizirani m’mene azimayi komanso ndoda zidatchenera, zidakakhala kuti adali ali choncho mumautoto a dziko zidakakhala zonyaditsa ndi zochititsa chidwi kwa wina aliyense? Poti akuti TVM tsopano imatha kufiikira kumayiko akutali, anthu ena akumayiko ena akamatiwona tiri thwanithwani mu mitundu ya zipani kodi akamatiwona azitiwona ngati ndani?

Iyi ndi nthawi yoti tizifunse makamaka pakakhala mwambo wa boma. Nthawi ya chipani chimodzi pamakhala mautoto a MCP wa chidali chipani chokhacho. Koma nthawi ino yomwe ndiyazipani zosiyanasiyana, tiyenera kumaganizira anthu azipani zina kuti.

Tiyenera kuzifunsa kuti kodi ndichifukwa chiani Malawi yemwe akaziwika ndika ndikugwirizana kwa anthu ndi chifukwa ninji lero akuziwika ndi mawu onyoza ndi mkangano. Chimozi mwa zinthu zomwe zapangitsa ndi kulowetsa ndale paliponse ndi pamene pomwe nkhani zandale siziyenera. Tiyeni tikonde dziko lathu.

No comments: